[Lyrics] Peoples Emcee – Nzeru

0
77

Intro
Nzeru nzeru nzeru 
Nzeru zangazi

PreChorus
Nzeru zanga ndizochepa
Ndimathedwa nzeru
Kwainu ndikopempha
Ndingopempha nzeru
Monga mfumu ijayo 
Ye inapempha nzeru

Chorus
Mundipatse nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundininkhe nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundipatse nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundininkhe nzeru
Ndingofuna nzeru

Verse 1
Sindikudziwa zanamachero
Kuno ndi kunja kunayanja lichero
Ndipatseni ufulu lero 
Dziko ndiukapolo
Ndakana uuzibalo
Ndakana unyambaro
Chiyambi cha nzeru ndikuopa inu
Ndi zakuya nzeru zanu
Palibe ofanana nanu
Mukhale nane ndikhale nanu
Lindigwire dzanja lanu
Chilichonse ndichanu
Ndikhalebe pamaso panu
Atate ine mwana wanu
Ndione mphamvu yanu
Atate ine mwana wanu
Ulemerero ndwanu
Atate ine mwana wanuNdidalira inu

PreChorus
Nzeru zanga ndizochepa
Ndimathedwa nzeru
Kwainu ndikopempha
Ndingopempha nzeru
Monga mfumu ijayo 
Ye inapempha nzeru

Chorus
Mundipatse nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundininkhe nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundipatse nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundininkhe nzeru
Ndingofuna nzeru

Verse 2
Zambiri padzikoli zothetsa nzeru
Nzeru zapadziko zimathetsa nzeru
Sindifuna kupenga ndi nzeru
Ndinu gwero la nzeru
Chinyengo, katangale ndi ziphuphu Zimandithetsa nzeruNjala, nthenda ndi nsanje
Zimandithetsa nzeru
Chilengedwe chanu chodabwitsa chimandithetsa nzeru
Mano amamera ndikusanduka magweru
Abwezi amasintha kusanduka adani
Ndikhulupirire ndani 
Padzikopa
Zambiri zokopa
Zisandichoke zokuopani
Mdimawu taunikani
Mdimawu taunikani

Bridge x2
Zopingazo ndithane nazo
Ndinu chitsanzo
Changa chisankho
Ndinu mayankho

PreChorus
Nzeru zathu ndizochepa
Timathedwa nzeru
Kwainu ndikopempha
Tingopempha nzeru
Monga mfumu ijayo 
Ye inapempha nzeru

Chorus
Mundipatse nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundininkhe nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundipatse nzeru
Ndingofuna nzeru
Mundininkhe nzeru
Ndingofuna nzeru

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here